Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:26 - Buku Lopatulika

26 koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Koma azithandiza abale ao m'chihema chamsonkhano ndi kumayang'anira ntchitoyo, koma asatumikire. Umu ndimo m'mene udzachitire poŵagaŵira ntchito zao Aleviwo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:26
10 Mawu Ofanana  

ndi kuti asunge udikiro wa chihema chokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.


Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira mu Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.


Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa chihema chokomanako, kuchita ntchito yonse ya chihema; koma mlendo asayandikize inu.


Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi;


Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa