Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Numeri 17:13 - Buku Lopatulika Yense wakuyandikiza chihema cha Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yense wakuyandikiza Kachisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati munthu aliyense amene akuyandikira chihema cha Chauta alikufa, ndiye kuti tonsefe ndife akufa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?” |
Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.
Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.
Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.
natsata munthu Mwisraele m'hema, nawapyoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.
Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.
Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.
Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.