Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:3 - Buku Lopatulika

3 Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 kupatula wokhawo umene uli pakati pake. Mulungu adanena kuti tisadye zipatso za mtengo umenewo, ngakhale kuzikhudza, chifukwa choti tikadzangotero, tidzafa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:3
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.


Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.


Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;


ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.


Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.


Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.


Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa