Numeri 18:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. Onani mutuwo |