Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 18:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:1
22 Mawu Ofanana  

Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.


Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.


Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.


“Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo.


“Chifukwa chiyani simunadyere pamalo wopatulika nsembe yopepesera machimo ija? Kodi imene ija siyopatulika? Kodi Yehova sanapereke nyamayo kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse powachitira mwambo wa nsembe yopepesera machimo pamaso pa Yehova?


ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’ ”


“ ‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.


Mudzavutika chifukwa cha machimo anu kwa zaka makumi anayi Chaka chimodzi chikuyimira tsiku limodzi la masiku makumi anayi amene munakazonda dziko lija ndipo mudzadziwa kuyipa kwake kwa kukangana ndi Ine.’


Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe.


Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?”


Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.


Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.


“Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.


“Bweretsa fuko la Levi ndipo ulipereke kwa Aaroni wansembe kuti lizimutumikira.


Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero.


Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni.


Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.


Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.


Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa