Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 16:14 - Buku Lopatulika

Ndiponso sunatilowetse m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yampesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuwonjezera apo, simudatiloŵetse m'dziko lamwanaalirenji, ndipo simudatipatse polima kapena minda yamphesa, kuti ikhale choloŵa chathu. Kodi mukufuna kutigwira m'maso? Ife sitibwera kumeneko.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”

Onani mutuwo



Numeri 16:14
12 Mawu Ofanana  

Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.


Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako;


koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.


ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.


Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.


Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa mu Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.


Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.


Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.