Numeri 20:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa mu Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ndipo chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito ndi kutifikitsa ku malo oipa ano? Kuno sikumera tirigu kapena mitengo ya mikuyu, kapena mitengo ya mipesa, kapenanso mitengo ya makangaza, ndipo kulibe ndi madzi akumwa omwe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!” Onani mutuwo |