Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 20:4 - Buku Lopatulika

4 Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chifukwa chiyani mwafikitsa mpingo wa Chauta kuchipululu kuno, kuti ife tifere kuno pamodzi ndi zoŵeta zathu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chifukwa chiyani unabweretsa gulu la Yehova mʼchipululu muno, kuti ife ndi ziweto zathu tife kuno?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 20:4
13 Mawu Ofanana  

Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao, amene anachita zazikulu mu Ejipito;


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?


Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


Koma m'mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.


Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.


pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m'chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa