Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 20:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa mu Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndipo chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito ndi kutifikitsa ku malo oipa ano? Kuno sikumera tirigu kapena mitengo ya mikuyu, kapena mitengo ya mipesa, kapenanso mitengo ya makangaza, ndipo kulibe ndi madzi akumwa omwe.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 20:5
8 Mawu Ofanana  

Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”


“Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti, “ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako, mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi, mmene unkanditsata mʼchipululu muja; mʼdziko losadzalamo kanthu.


Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti, amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma ndi lokumbikakumbika, mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima, dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’


Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova.


Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”


“Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba.


chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).


Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa