Eksodo 22:5 - Buku Lopatulika5 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 “Munthu akamalekerera zoŵeta zake kuloŵa m'munda mwa munthu wina ndi kukadya mbeu za m'mundamo, mwini zoŵetayo alipire mbeu zabwino kwambiri za m'munda mwake, kapena mphesa zake zabwino kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Ngati munthu alekerera ziweto zake kukalowa mʼmunda wa munthu wina kukadya mbewu zake, munthuyo amubwezere mwini mundawo mbewu zina zabwino kapena mpesa wina wabwino kwambiri. Onani mutuwo |