Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:6 - Buku Lopatulika

6 Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Moto ukabuka mpaka kukafika ku thengo, ndipo ukatentha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula kapena munda umene uli ndi mbeu, amene adatenthayo alipire zoonongekazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:6
8 Mawu Ofanana  

Koma ngati chidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo.


Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.


Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibedwa m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.


Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.


Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa