Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 22:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Ngati munthu alekerera ziweto zake kukalowa mʼmunda wa munthu wina kukadya mbewu zake, munthuyo amubwezere mwini mundawo mbewu zina zabwino kapena mpesa wina wabwino kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Munthu akamalekerera zoŵeta zake kuloŵa m'munda mwa munthu wina ndi kukadya mbeu za m'mundamo, mwini zoŵetayo alipire mbeu zabwino kwambiri za m'munda mwake, kapena mphesa zake zabwino kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:5
7 Mawu Ofanana  

Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.


mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho.


Koma ngati chiwetocho chinabedwa, iye ayenera kubwezera mwini wakeyo.


Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.


“Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho.


“Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire.


Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa