Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 16:13 - Buku Lopatulika

13 kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kodi zikukucheperani kuti mudatitulutsa ku dziko lamwanaalirenji ku Ejipito, kuti tifere m'chipululu muno? Kodi mukufunanso kuti mukhale mfumu yathu yotilamula?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:13
19 Mawu Ofanana  

Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?


koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?


Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?


Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;


Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Ejipito?


Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa