Numeri 16:10 - Buku Lopatulika ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? Ndipo kodi mufunanso ntchito ya nsembe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? Ndipo kodi mufunanso ntchito ya nsembe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiponso kodi Mulungu adakulolani kuti mubwere pafupi ndi Iye, inu pamodzi ndi abale anu Alevi, amene ali nanu? Kodi mukukhumbiranso ndi unsembe womwe? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe. |
Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.
Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.
Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.
Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m'nyumba ya Mika.