Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono iwe pamodzi ndi ana ako, muzitumikira pa ntchito zaunsembe, ntchito zonse zokhudza guwa, ndi pa ntchito zonse za m'malo opatulika kwambiri. Ndakupatsa unsembe ngati mphatso yako, koma munthu wina aliyense wofika pafupi, adzaphedwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:7
28 Mawu Ofanana  

Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao.


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.


Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;


iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.


Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.


ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.


Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;


Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele.


Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa chihema chonse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.


Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.


Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.


Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.


Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.


Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.


Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum'mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa