Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 16:9 - Buku Lopatulika

9 kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku gulu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya chihema cha Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku khamu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya Kachisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:9
20 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.


Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu!


Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.


Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.


Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?


Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?


iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?


Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;


Sendera nalo kuno fuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.


Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.


Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.


Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa