Numeri 16:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira? Onani mutuwoBuku Lopatulika9 kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku gulu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya chihema cha Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku khamu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya Kachisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo? Onani mutuwo |
Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi.