Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 15:31 - Buku Lopatulika

Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Popeza kuti wanyoza mau a Chauta ndipo waphwanya lamulo la Chauta, amchotseretu munthu ameneyo, tchimo lake lidzamkangamira.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ”

Onani mutuwo



Numeri 15:31
19 Mawu Ofanana  

Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.


popeza anapikisana nao mau a Mulungu, napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;


Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu.


Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Wonyoza mau adziononga yekha; koma woopa malangizo adzalandira mphotho.


Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo;


Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.


Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,


ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa;


Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.


Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;


Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.


Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.


Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.