Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
Numeri 14:41 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mose adati, “Chifukwa chiyani mukunyoza lamulo la Chauta, poti zimenezo sizidzatheka? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Mose anati, “Chifukwa chiyani simukumvera lamulo la Yehova? Zimenezi sizitheka! |
Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.
ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?
Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.
Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?