Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 32:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Zedekiya adzatengedwa kupita ku Babiloni, ndipo adzakhala kumeneko mpaka nditamkhaulitsa, akutero Chauta. Ngakhale iye adzamenyane nawo chotani Ababiloniwo, sadzatha kuŵapambana.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Zedekiya adzatengedwa kupita naye ku Babuloni, kumene adzakhale mpaka nditamukhawulitsa, akutero Yehova. Ngakhale iye adzamenyane ndi Babuloni, koma sadzapambana.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:5
20 Mawu Ofanana  

Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.


Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.


adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.


taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.


Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,


Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mzinda uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.


Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.


Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.


Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.


Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m'zigologolo, kunka naye ku Babiloni.


Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.


Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake.


Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.


Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?


Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa