Numeri 14:32 - Buku Lopatulika Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma enanu, mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu mommuno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma inu mitembo yanu idzakhala ngundangunda mʼchipululu muno. |
mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;
Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.
Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?