Numeri 14:33 - Buku Lopatulika33 Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'chipululu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'chipululu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Ana anu adzakhala abusa m'chipululu akungoyendayenda zaka makumi anai, ndipo adzasauka chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka inuyo mutatha ndi kufa m'chipululu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu muno zaka makumi anayi, kuvutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka munthu womaliza mwa inu atafa mʼchipululu muno. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.