Numeri 14:1 - Buku Lopatulika Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo mpingo wonse udafuula kwambiri, ndipo anthu adalira usiku umenewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri. |
Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.
Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.
Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.
Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!
Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu.
Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.
Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.
Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.