Numeri 13:30 - Buku Lopatulika Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Kalebe adaŵakhalitsa chete anthu pamaso pa Mose, nati, “Tiyeni tipite nthaŵi yomwe ino, tikalande dzikolo, chifukwa tingathe kuligonjetsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.” |
Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.
Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitingathe kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu.
koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.
amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,