Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
Numeri 12:10 - Buku Lopatulika Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtambo utachoka pamwamba pa chihema, Miriyamu adapezeka ali ndi khate lambuu ngati ufa, ndipo Aroni atacheuka, adangoona Miriyamu ali ndi khate. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mtambo unachoka pamwamba pa Chihema, taonani, Miriamu anagwidwa ndi khate. Aaroni atachewuka anaona Miriamu ali ndi khate; |
Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.
Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.
Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.
Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;
Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:
Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriyamu panjira, potuluka inu m'dziko la Ejipito.