Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Chauta adailanga mfumuyo ndi nthenda ya khate mpaka kufa kwake, ndipo inkakhala m'nyumba yakeyake yapadera. Choncho Yotamu mwana wa mfumuyo ndiye amene ankayang'anira banja la mfumu, namalamulira anthu m'dzikomo m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:5
20 Mawu Ofanana  

chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.


Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse.


Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.


Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?


Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake,


Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a chibadwidwe chao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobowamu mfumu ya Israele.


Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.


Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono.


Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.


Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.


Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa