Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 12:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pamene mtambo unachoka pamwamba pa Chihema, taonani, Miriamu anagwidwa ndi khate. Aaroni atachewuka anaona Miriamu ali ndi khate;

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mtambo utachoka pamwamba pa chihema, Miriyamu adapezeka ali ndi khate lambuu ngati ufa, ndipo Aroni atacheuka, adangoona Miriyamu ali ndi khate.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 12:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.


Khate la Naamani lidzakumatirira iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Ndipo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa ali ndi khate lotuwa ngati phulusa.


Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa?


Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa.


Ngakhale atalera ana ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire. Tsoka kwa anthuwo pamene Ine ndidzawafulatira!


“Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.


“Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake.


Kumbukirani zimene Yehova Mulungu wanu anachita kwa Miriamu muli paulendo mutatuluka mu Igupto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa