Numeri 11:26 - Buku Lopatulika Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa. |
Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.
Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?
Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono.
Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.
Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.
ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.