Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Numeri 11:18 - Buku Lopatulika Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino mu Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino m'Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uŵauze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera zamaŵa, ndipo mudzadya nyama. Inuyo mudalira Chauta alikumva, pamene munkati, “Ndani atipatse nyama tidye? Paja zinthu zinkatiyendera bwino ku Ejipito.” Nchifukwa chake Chauta adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. |
Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.
Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako ndi mitsinje inasefuka; kodi adzakhozanso kupatsa mkate? Kodi adzafunira anthu ake nyama?
Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;
amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,
Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sungathe kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.
Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.