Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:39 - Buku Lopatulika

39 amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 “Koma makolo athu aja adakana kumumvera, m'malo mwake adamkankhira kumbali. Mitima yao idatembenukira za ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 “Koma makolo athu anakana kumumvera iye. Iwo anamukana iye ndipo mʼmitima mwawo anatembenukira ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:39
15 Mawu Ofanana  

Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.


Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;


Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.


Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?


ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;


Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa