Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Numeri 1:7 - Buku Lopatulika Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa fuko la Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda, |
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda: