Koma oyang'anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;
Numeri 1:5 - Buku Lopatulika Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maina a anthu okuthandizaniwo ndi aŵa: fuko la Rubeni, akuthandizeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni, |
Koma oyang'anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;
Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.
Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:
akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;