namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.
Numeri 1:32 - Buku Lopatulika A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.
Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.
Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.
Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi.
owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.
Ndipo za Yosefe anati, Yehova adalitse dziko lake; ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame, ndi madzi okhala pansipo;
Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.