Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:33 - Buku Lopatulika

33 owerengedwa ao a fuko la Efuremu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 owerengedwa ao a fuko la Efuremu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Efuremu, adapezeka kuti ali 40,500.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:33
7 Mawu Ofanana  

Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.


Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa