Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 46:20 - Buku Lopatulika

20 Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Manase ndi Efuremu anali ana amene Yosefe adabereka mwa Asenati, mwana wa Potifera wansembe wa ku Oni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:20
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito.


Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini.


Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.


Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.


Anyamata a Oni ndi Pibeseti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.


Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.


Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa