Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 1:32 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

32 A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:32
14 Mawu Ofanana  

Iye anamutcha mwanayo Yosefe, ndipo anati, “Mulungu andipatsenso mwana wina.”


Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.


Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ”


Anthu ochokera ku Negevi adzakhala ku mapiri a Esau, ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri adzatenga dziko la Afilisti. Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya, ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.


Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.


Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.


Za fuko la Yosefe anati: “Yehova adalitse dziko lake ndi mame ambiri ochokera kumwamba ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;


Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa