Obadiya 1:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Ayuda akumwera adzalandira phiri la Esau, akuzambwe adzalandira dziko la Afilisti. Akumpoto adzalandira dziko la Efuremu ndi likulu lake Samariya, ndipo Abenjamini adzalandira dziko lakuvuma la Giliyadi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Anthu ochokera ku Negevi adzakhala ku mapiri a Esau, ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri adzatenga dziko la Afilisti. Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya, ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi. Onani mutuwo |
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.