Obadiya 1:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala mu Sefaradi adzakhala nayo mizinda ya kumwera, cholowa chao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwera, cholowa chao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Aisraeli amene ali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati; a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda ya ku Negevi. Onani mutuwo |
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.