Nehemiya 7:3 - Buku Lopatulika
Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala mu Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.
Onani mutuwo
Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.
Onani mutuwo
Tsono ndidaŵauza kuti, “Musalole kuti atsekule zipata za Yerusalemu mpaka dzuŵa litatentha. Ndipo atseke zitseko ndi kuzipiringidza, alonda asanaŵeruke. Musankhe olonda pakati pa anthu okhala m'Yerusalemu, aliyense akhale pamalo pake, ndiponso akhale poyang'anana ndi nyumba yake.”
Onani mutuwo
Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
Onani mutuwo