Nehemiya 3:23 - Buku Lopatulika23 Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Pambali pa iwowo Benjamini ndi Hasubu adakonza chigawo china choyang'anana ndi nyumba zao. Pambali pa iwowo Azariya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Ananiya, adakonza chigawo china pafupi ndi nyumba yake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.