Nehemiya 13:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Nchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuziyamba kuda, tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Onani mutuwo |