Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:4 - Buku Lopatulika

4 Mzindawo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mudziwo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu, koma anthu okhala mumzindamo anali oŵerengeka, ndipo munalibe nyumba zambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:4
7 Mawu Ofanana  

Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.


Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala mu Yerusalemu.


Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala mu Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.


Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.


Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa