Nehemiya 7:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono Mulungu adaika mumtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse atsogoleri, akuluakulu ndiponso anthu onse, kuti alembedwe potsata mibadwo ya mabanja ao. Ndidapeza buku m'mene mudalembedwa maina a mabanja a anthu amene anali oyamba kubwerako ku ukapolo. Zolembedwa m'menemo zinali izi: Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo: Onani mutuwo |