ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
Nehemiya 2:1 - Buku Lopatulika Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mwezi wa Nisani, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene adabwera ndi vinyo pamaso pa mfumuyo, ndidatenga vinyoyo ndi kumpereka kwa mfumu. Tsono nkale lonse sindidakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. |
ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao.
Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.
Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.
Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.
Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.