Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 7:7 - Buku Lopatulika

7 Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi Anetini, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Arita-kisereksesi, Ezarayo adanyamuka kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Aisraele ena, ndiye kuti ansembe ndi Alevi, oimba nyimbo, alonda ndiponso anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tsono mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wa Aritasasita, Ezara pamodzi ndi Aisraeli ena, kuphatikizapo ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda, ndi anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ananyamuka kubwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 7:7
14 Mawu Ofanana  

Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.


Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m'kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.


Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.


Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,


Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m'kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,


Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,


Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa