Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
Nehemiya 11:3 - Buku Lopatulika Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele wamba ambiri, pamodzi ndi ansembe, Alevi, anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso zidzukulu za atumiki a Solomoni, onsewo ankakhala m'midzi mwao, aliyense m'dera la choloŵa chake. Koma akuluakulu a m'chigawo cha Yuda anali atakhazikika ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu. |
Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisraele onse m'midzi mwao.
Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'cholowa chake.
Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;
Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.
Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo:
Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi antchito a m'kachisi, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao.