Nehemiya 10:9 - Buku Lopatulika Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alevi anali aŵa: Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi, wa fuko la Henadadi, Kadimiyele, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alevi anali awa: Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli, |
Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.
Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.
Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya.
Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.
Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao.