Nehemiya 9:4 - Buku Lopatulika4 Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau akulu kwa Yehova Mulungu wao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Pa makwerero okhalapo Alevi padaimirira Yesuwa, Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Onsewo ankapemphera mokweza mau kwa Chauta, Mulungu wao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.