Nehemiya 12:24 - Buku Lopatulika24 Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Atsogoleri a Alevi, Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ankathandizana ndi abale ao poimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza, monga momwe Davide, munthu wa Mulungu, adaaŵalamulira kuti gulu liziimba molandizana ndi gulu linzake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira. Onani mutuwo |
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.