Mlaliki 4:3 - Buku Lopatulika inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wopambana onsewo ndi amene sadabadwe nkomwe, ndipo ntchito zoipa zimene zimachitika pansi pano sadaziwone. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma wopambana onsewa ndi amene sanabadwe, amene sanaone zoyipa zimene chimachitika pansi pano. |
Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.